1 Samuel 3

Yehova Ayitana Samueli

1Samueli ankatumikira Yehova moyangʼaniridwa ndi Eli. Masiku amenewo mawu a Yehova sankamveka pafupipafupi. Kuona zinthu mʼmasomphenya sikunkachitikanso kawirikawiri.

2Tsiku lina Eli, amene maso anali ofowoka ndi kuti sankatha kuona bwino, anagona pa malo ake. 3Nthawiyi nʼkuti nyale ya Mulungu isanazimitsidwe. Samueli anali gone mu Nyumba ya Yehova, kumene kunali Bokosi la Chipangano cha Mulungu. 4Yehova anayitana Samueli.

Iye anayankha kuti, “Wawa.”
5Ndipo iyeyo anathamangira kwa Eli ndipo anati, “Ndabwera ndamva kuyitana.”

Koma Eli anati, “Ine sindinakuyitane, bwerera kagone.” Ndipo iye anapita kukagona.

6Yehova anayitananso, “Samueli!” Ndipo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli nati, “Ndabwera popeza ndamva mukundiyitana.”

Eli nati, “Mwana wanga, ine sindinakuyitane, bwerera kagone.”

7Nthawiyi nʼkuti Samueli asanadziwe Yehova ndipo Mawu a Yehova nʼkuti asanawululidwe kwa iye.

8Yehova anayitananso Samueli kachitatu ndipo Samueli anadzuka ndikupita kwa Eli ndipo anati, “Ndabwera popeza mwandiyitana ndithu.”

Apo Eli anazindikira kuti Yehova ndiye ankayitana mnyamatayo.
9Tsono Eli anamuwuza Samueli kuti, “Pita ukagone ndipo akakuyitananso ukanene kuti, ‘Yankhulani Yehova, pakuti mtumiki wanu ndikumvetsera.’ ” Choncho Samueli anapita ndi kukagona pamalo pake.

10Yehova anabwera ndi kuyima pomwepo, ndi kuyitana monga nthawi zina zija, “Samueli! Samueli!”

Ndipo Samueli anayankha, “Yankhulani, pakuti mtumiki wanu akumvetsera.”

11Ndipo Yehova anati kwa Samueli, “Taona, patsala pangʼono kuti ndichite chinthu china mu Israeli chimene chidzadabwitsa aliyense amene adzamve. 12Tsiku limenelo ndidzachitadi zonse zimene ndinayankhula zokhudza banja la Eli kuyambira poyamba mpaka pomaliza. 13Pakuti ndinamudziwitsa kuti Ine ndikhoza kulanga banja lake kwamuyaya chifukwa cha zoyipa zimene ana ake ankadziyipitsa nazo. Iye ankadziwa zimenezi koma osawaletsa. 14Nʼchifukwa chake ndinalumbira kuti, ‘Zoyipa zimene banja la Eli linandichita sizidzafafanizidwa mpaka muyaya ngakhale adzapereke nsembe kapena zopereka zina.’ ”

15Samueli anagona mpaka mmawa. Atadzuka anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova. Iye anachita mantha kumuwuza Eli za masomphenya ake. 16Koma Eli anamuyitana nati, “Samueli mwana wanga.”

Samueli anayankha kuti, “Wawa.”

17Tsono Eli anafunsa kuti, “Yehova wakuwuza chiyani? Usandibisire. Mulungu akulange ndithu ngati undibisira chilichonse cha zimene wakuwuza.” 18Choncho Samueli anamuwuza zonse, sanamubisire kalikonse. Ndipo Eli anati, “Iye ndi Yehova, mulekeni achite chimene chamukomera.”

19Yehova anali ndi Samueli pamene amakula, ndipo zonse zimene ankayankhula zinkachitikadi. 20Ndipo Aisraeli onse kuyambira ku dera la Dani mpaka ku Beeriseba anazindikira kuti Yehova analozadi chala pa Samueli kuti akhale mneneri wake. 21Yehova anapitiriza kuoneka ku Silo, ndipo kumeneko anadziwulula yekha kwa Samueli mwa mawu ake.

Copyright information for NyaCCL